ATSOGOLERI APEMPHEDWA KUTSATIRA MFUNDO ZA DEMOKALASE PAMENE MISONKHANO YOKOPA ANTHU YAYAMBIKA.

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCathy Chakwera wapempha anthu kukhala ololerana komanso kulemekeza ufulu wa ena pomwe nyengo ya kampeni yatsegulidwa.

Dr Chakwera anena izi lolemba pa 14 July, 2025 madzulo, pomwe amayankhula kufuko la aMalawi kunyumba yachifumu ya Sanjika mumzinda wa Blantyre.

Iwo ati kwa onse omwe akupikisana mipando yosiyanasiyana apewe kuyankhula mawu otonza amzawo kaamba koti mchitidwe oterewu umabweretsa udani omwe umadzetsa kugawanika zomwe mapeto ake zimayambitsa ziwawa.

Ndipo ati munyengo yokopa anthuyi, kwa onse omwe azipezeka akuyambitsa kapena kukolezera mchitidwe wazipolowe, apolisi adzagwira ntchito yawo kaamba koti ndizotsutsana ndi ngodya zaulamuliro wa demokalase.

Related posts

https://umoyofm.mw/tigwirizane-polimbana-ndi-hiv/

TIGWIRIZANE POLIMBANA NDI HIV

ANTHU APEMPHEDWA KUSINTHA KAGANIZIDWE PA ZAMATENDA OSAPATSIRANA.

1 comment

Hank2849 August 6, 2025 - 11:47 am
Add Comment